Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Chipani cha MCP mchachitukuko — Kabwila

Mneneri wa chipani cha MCP, a Jessie  Kabwila, wati dziko la Malawi likusintha kwambiri pa chitukuko.

Poyankhula pamsonkhano wa atolankhani ku Lilongwe komwe akufotokoza za momwe udayendela msonkhano waukulu wa chipani cha MCP, a Kabwila ati ndizosangalatsa kuona kuti sitima yayambanso kuyenda m’dziko muno patatha zaka 21.

Mwa zina, iwo ati chipani cha MCP chidasankha anthu otha kutchakula mfundo kapena kuti kutipula monga momwe adapemphera Prezidenti Chakwera pomwe chipanichi chikukonzekela chisankho cha 2025.

A Kabwila ati mtsogoleri wa dziko lino akudzipereka pokweza miyoyo ya alimi, omwe anati chaka chino agulitsa fodya wawo pa mitengo yabwino.

Iwo anati ntchito yokonza misewu ipitilira, yomwe ndi gwelo lalikulu la zachuma.

Print Friendly, PDF & Email

Author

  • Mayeso Chikhadzula joined MBC in 2006, he's an Investigative Journalist and Principal Reporter. He's also a News Anchor, Presenter, and producer.

Related posts

MULTICHOICE DONATES TV SPORTS BROADCASTING EQUIPMENT TO MBC

MBC Online

“A Gotani – Hara ali ndi luntha potsogolera” — President Chakwera

Timothy Kateta

Dr Usi ati adzipereka pofuna kukweza miyoyo ya a Malawi

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.