Mtsogoleri wa zokambirana mu nyumba ya malamulo, a Richard Chimwendo Banda, wayamika mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera chifukwa chokhala ndi chikhulupiliro mwa amayi pamene adasankha a Catherine Gotani Hara kukhala sipikala oyamba wachizimayi mnyumbayi.
A Chimwendo Banda ati President Chakwera wakhala akusankha amayi ambiri m’maudindo akuluakulu ndipo aMalawi akuyenera kutengera zimenezi pomakhulupilira amayi.
Iwo ati a Gotani Hara agwira ntchito yabwino kwambiri m’zaka zisanu zapitazi yotsogolera Nyumba ya Malamulo.
Pamenepa, a Chimwendo Banda anapempha aphungu onse kuti ayime ndi kupereka ulemu wapadera kwa a Catherine Gotani Hara.
Iwo ayamikanso Dr Lazarus Chakwera chifumwa chowasankha kukhala mtsogoleri wa zokambirana m’nyumbayi.
A Richard Chimwendo Banda ayamikanso Dr Chakwera chifukwa chokwaniritsa malamulo, pomabwera ku nyumba ya malamulo kudzayankha mafunso kuchoka kwa aphungu.
Iwo ati kupatulapo mtsogoleri wakale wa dziko lino, Dr Bakili Muluzi, amene adakayankhapo mafunso kamodzi ku nyumbayi, palibenso mtsogoleri wina amene adachitako zimenezi koma Dr Chakwera okha basi.
A Chimwendo Banda anayamikiranso Dr Chakwera chifukwa chokweza ndalama za Constituency Development Fund kuchokera pa K40 million kufika pa K200 million kwacha, zimene zathandiza kubweretsa chitukuko m’madera onse a aphungu m’dziko muno.
Pa nkhani ya ophunzira a m’sukulu za ukachenjede, iwo ati ophunzira 30,000 akuthandizidwa ndi boma powapatsa fizi ndi ndalama ya sopo, zimene sizinayambe zachitikapo.
Olemba: Isaac Jali