Oyimba nyimbo za uzimu, mayi busa Mary Thuya, ati chimbale chimene akutulutsa chotchedwa “Ndathokoza” ayimba pothokoza Mulungu kaamba kowachiritsa ku matenda a Covid-19.
A Thuya anena izi pokonzekera mwambo okhazikitsa chimbalechi, umene udzakhalepo Lamulungu likudzali munzinda wa Lilongwe.
Iwo ati anthu amene adzapite kumwambowu ayembekezere kukalimbikitsika kudzera ku umboni wawo.
Oyimba ena amene akaimbe nawo ndi monga Sir Norman Phiri, Favoured Martha, Alex Nkalo, Milefa Sisters komanso Maxwell Oloto.