Mmodzi mwa akatswiri pa nkhani za utsogoleri ndi ufulu wachibadwidwe, a Undule Mwakasungula, wati ganizo la chipani cha UTM lofuna kutuluka mu mgwirizano wa Tonse lachitika pa nthawi yolakwika ndipo litha kusokoneza tsogolo lachipanichi.
Mu chikalata chomwe atulutsa, Mwakasungula ati chipanichi chikanachilimika posankha mtsogoleri watsopano komanso kupeza njira zina zokonzera mavuto awo mu mgwirizano wa Tonse.
Iwo ati ganizoli lili ndi kuthekera kogawa chipanichi.
Iwo ati utsogoleri wa Malemu Dr Saulos Chilima unali olunzanitsa anthu otsatira chipanichi mokomera chitukuko cha dziko lino.
Malinga ndi a Mwakasungula, chipanichi chisokonekera ngati sichiyenda mosamala ndikugumula maziko amene malemu Dr Chilima anawavutikira kumanga.
Olemba: Blessings Cheleuka