Nduna yoona kuti pasamakhale kusiyana pantchito pakati pa amuna ndi akazi, a Jean Sendeza, ati kukhazikitsidwa kwa mtukula pakhomo wa m’mizinda ndi chitsimikizo choti mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, wadzipereka kuonetsetsa kuti anthu apeze popumira pamene boma likukonza chuma cha dziko lino.
Mai Sendeza anena izi ku Zomba kumene ntchito yokhazikitsa mtukula pakhomo wa m’mizinda ya K15.7 billion ili mkati.
Iwo apempha anthu omwe akusankha opindula kuti asamakondere palembana maina.