Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani Politics

Chakwera acheza ndi anthu munzinda wa Lilongwe

Popitiriza kucheza ndi aMalawi m’madera osiyanasiyana, Prezidenti wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera masana ano acheza ndi anthu m’madera angapo munzinda wa Lilongwe.

Dr Chakwera akuchita zimenezi pofuna kuwafotokozera anthu ntchito zachitukuko zomwe boma likugwira m’madera osiyanasiyana komanso zomwe likuchita pofuna kuthandiza anthu pa mavuto awo monga njala kaamba ka ng’amba yomwe idagwa kumayambiliro a chaka chino.

Prezidenti wa dziko linoyu akumalimbikitsanso anthu kukalembetsa mukaundula wa voti pokonzekera chisankho cha chaka cha mawa.

Mwa madera ena, Dr Chakwera acheza ndi anthu ku Area 23, Kawale, Area 24, kwa Kandikole ku Area 36, kwa Chinsapo 1, Mtandile, Area 49, Area 25, pa Lilongwe TTC komanso kwa Kauma.

Pakadali pano, khwimbi lasonkhana kale pa Area 23, pomwe Dr Chakwera akuyembekezeka kufika posachedwapa.

Related posts

Malawi set to host ANOCA Zone VI Elective AGM

Yamikani Simtowe

MCCCI Business Leaders Summit receives boost from Britam Insurance

Alinafe Mlamba

GOVERNMENT REDUCES THE PRICE OF PETROL

McDonald Chiwayula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.