Nthambi yaza ndende mchigawo chakummwera yati chaka cha 2024 chakhala chopambana mukagwiridwe kawo ka ntchito.
Izi ndi malinga ndi mkulu wa nthambiyi mchigawochi, a Zacheus M’bawa.
Poyankhula pa mwambo osangalalira mmene nthambiyi yagwilira ntchito, a M’bawa ati m’chakachi, mwazina, achepetsa chiwerengero cha akaidi othawa mndende, alimbikitsa ulimi wambewu ndi ziweto komanso alimbikitsa ntchito zoonetsetsa kuti anthu amene anali ku ndende akulandiridwa bwino mmadera awo akamaliza kugwira zilango zawo.
Pamenepa, iwo ati m’chaka chikudzachi cha 2025 alimbikitsa ntchito za ulimi mndende za Mwanza, Bvumbwe ndi Mulanje kuti nthambiyi ipitilire kukhala yodzidalira kugawo la chuma ndi chakudya.
Pamwambowu, umene unachitikira ku Mulanje, panafika ogwira ntchito zandende ochokera ku Chikwawa, Thyolo, Bvumbwe ndi Nsanje.
Gulu loimba la Prison Strings Band ndilomwe linasangalatsa anthuwa usiku onse.
Olemba: Geoffrey Chinawa