Unduna wazamaboma ang’ono wapereka makina apamwamba osiyanasiyana opangira mafuta ophikira a ndalama zokwana $90,000 ku gulu la alimi la BOMFA ku Kasungu.
Makinawa akuyembekezeka kupititsa patsogolo ntchito yopanga mafuta a mpendadzuwa, omwe alimiwa amalima mdera la Senior Chief Mphomwa m’bomali.
Wachiwiri kwa nduna ya zamaboma ang’ono, a Joyce Chitsulo, ati masomphenya a boma ndikulimbikitsa alimi ang’onoang’ono kuchita ulimi wa bizinesi.
A Chitsulo ati boma likufuna kuti aMalawi adzipanga okha katundu osiyanasiyana mmalo mogwiritsa ntchito ndalama zakunja kukagulira katunduyu.
Makinawa awagula pansi pa ntchito ya Transforming Agriculture through Diversification and Entrepreneurship (TRADE).
Mkulu wa ntchitoyi, a Francis Sakala, ati pakadalipano akhazikika pogula makina komanso kumanga mafakitale kuti magulu a alimiwa adzipanga katundu wapamwamba, yemwe adzitha kumugulitsa pa msika mosavuta.
Malinga ndi mkulu wa gulu la alimi la BOMFA, a Zaina Kapachika, pachaka amapanga malita 50,000 a mafuta ophikira omwe amagulitsa mderali ndipo ati makinawa awathandiza kuchulutsa ndi kuwakonza mafutawa kuti ayambe kupezeka msitolo zikuluzikulu m’dziko muno.
Kupatula makina opangira mafutawa, guluri lalandiranso makina omwe adzitha kupangira sopo komanso zakudya za ziweto ku zotsalira za mpendadzuwa.