Malawi Broadcasting Corporation
Crime Local Nkhani

Bandera ali mchitokosi pomuganizira kuti anazembetsa mtsikana wachichepere

Apolisi ku Mangochi amanga oyimba odziwika kuti Bandera koma dzina lake lenileni ndi Abdul-Karim Saidi pomuganizira kuti anasunga mokakamiza mtsikana wachichepere wazaka 14.

Ofalitsankhani za polisi ya Mangochi, Amina Tepani Daudi, watsimikiza zankhaniyi.

Iye wati malipoti owe ali nawo akusonyeza kuti Bandera anayamba ubwenzi ndi mtsikanayu miyezi itatu yapitayo ndipo usiku wapa 2 January anatengana ndi mtsikanayu kupita naye kwawo kumene anakana kugona ndipo mmalo mwake anapita naye kumalo ogona alendo komwe anagonako masiku awiri.

“Malipoti akusonyezanso kuti mayi ake a mtsikanayu mumasiku awiri amenewa amayesetsa kuimba telefoni yake ya mmanja ya mtsikanayo  koma simayankhidwa ndipo Bandera anawayimbira mayiwo kuwauza kuti asadandaule kalikonse,” watero Daudi.

Malinga ndi a Daudi, mayiwo mothandizana ndi achibale anagwirizana kuti akumane naye Bandera ndipo atangokumana anamugwira ndikukamupereka ku polisi, kumene amutsegulira mulandu osunga munthu mokakamiza.

Bandera wati cholinga chake amafuna ajambule naye mtsikanayo kanema wanyimbo yake yatsopano.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

MANEB lauded for digitalising access to examination results

Chisomo Break

A Likhutcha alimbikitsa bata

Mayeso Chikhadzula

Child obesity can reduce life expectancy — Nutritionist

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.