Timu ya Ekhaya tsopano ili ndi mwayi waukulu olowa mu ligi yaikulu ya TNM kuchoka mu ligi ya mchigawo chakummwera pomwe tsopano ikungofuna ma poinsi awiri pamaseweronso awiri amene yatsalanawo.
Timuyi lero yagonjetsa timu ya Wanderers Reserve ndizigoli ziwiri kwa duu, zimene zapangitsa kuti idzitsogola ndi ma poinsi asanu kutsatira kulepherana kwa matimu a Red Lions ndi Nyambadwe United pamasewero enanso omwe aseweredwa masana a lolemba.
Ekhaya ili ndi ma poinsi 28 pomwe Red Lions yomwe ndiyachiwiri ili ndi ma poinsi 23 ndipo onse atsala ndi masewero awiri kuti amalize ligi ya Thumbs Up.
Red Lions ikuyembekezeka kusewera ndi Ntaja United komanso Wanderers Reserve pamasewero ake omaliza pomwe Ekhaya yatsala ndi matimu a Nyambadwe United ndi Nyasa Big Bullets Reserve.
Ngati Ekhaya ingapambane masewero ake otsatira kapena kufananitsa mphamvu masewero onse awiri ndiye kuti ikhala akatswiri pomwe Red Lions ikuyenera kupambana masewero onse komanso kuti Ekhaya igonje masewero onse otsala kuti asilikali aku Zombawa abwererenso mu ligi ya TNM.