Gulu la akatswiri oyimba nyimbo zauzimu osachepera 50 amene adakumana koyamba mu 2020, tsopano akhazikitsa Hephzibah Worship Band.
Malinga ndi mkulu wa gululi a Peterson Nachanje, cholinga cha gululi ndi kusula komanso kutukula luso lamayimbidwe auzimu.
“Sitikusiyana kwenikweni ndi Joyous Celebration yaku South Africa. Sitikuona mpingo koma luso lamunthu, kaya amatha kuimba zida kaya mawu, ali olandiridwa abwere,” atero a Nachanje.
M’modzi mwa otsogolera gululi ndi Good Friday, yemwe anatchuka ndi nyimbo yoti ‘Wanga ndili Naye’ ndipo wati gululi linayamba kujambula chimbale m’chaka cha 2021 ndipo pofika lero lajambula akanema atatu apamwamba.
Wolemba: Emmanuel Chikonso