Bungwe la maiko akumwera kwa mu Africa la Southern Africa Development Community (SADC) lati mphepo ya El Niño yadzetsa mavuto ambiri omwe akhudza anthu opitilira 61 million a mchigawocho.
Atsogoleri a mmaikowa amayankhula izi pa msonkhano wawo wa pa kanema okhudza vutoli, omwe anali nawo pa 20 May, 2024.
Anatsogolera zokambiranazo ndi President wa dziko la Angola a João Manuel Lourenço, yemwenso ndi wampando wa bungweli, ndipo agwirizana njira zofuna kupeza ngakhalenso kupempha ndalama yokwana $5.5 billion kuti athandize nzika za mchigawochi zomwe zakhudzidwa kwambiri ndi vutoli, lomwe ladza chifukwa cha ng’amba komanso kusefukira kwa madzi.
Bungweli lapemphanso maiko onse achigawochi kuti aike ndondomeko zoyenera zothana ndi mphepo ya La Niña yomwe ikuyembekezeka kudzachitika chaka cha mawa.
Nduna yoona za kunja kwa dziko lino, a Nancy Tembo, anatenga nawo mbali pa msonkhanowu.
Olemba: Alufisha Fischer