Pali kusamvana kunyumba ya malamulo pomwe aphungu akumbali yaboma ndi otsutsa akulephera kugwirizana kuti akambirane za kusintha kwa lamulo lakagulidwe ka mafuta agalimoto m’dziko muno.
Nduna yaza magetsi ,a Ibrahim Matola, abweretsa bill yomwe akuitchula kuti “Energy Regulation Amendment Bill” muchizungu imene sinakwanitse masiku 21 omwe akhoza kukambirana.
Koma malingana ndi malamulo anyumbayi aphungu amayenela kuponya voti kuvoneleza kuti akambirane bill yotele. Apa ndipomwe aphunguwa sakumvana kaamba kokuti mbali ya aphungu otsutsa sakufuna kukambirana za lamuloli.
Mtsogoleri wa zokambirana mnyumbayi, a Richard Chimwendo Banda, komabe auza aphunguwa kuti ngakhale akuchita dala mpungwepungwe bilu imeneyi ayikambirana lero poti ndi yofunika pa ntchito yogula mafuta agalimoto zomwe a Malawi ambiri akufuna zidziyenda bwino.
Kuyambira mmawa pomwe alowa half past 9 mnyumbayi, aphunguwa sanakambiranepo chili chonse.
Pakadali pano aphunguwa akuvota kachiwiri chiyambire nkhaniyi.