Malawi Broadcasting Corporation
Health Local Local News Nkhani

Aphungu akufuna mowa, fodya zikhale ndi misonkho

Aphungu a nyumba ya malamulo ati pakufunika kuonjezera msonkho pa mowa ndi fodya kuti padzipezeka ndalama zothandizira polimbana ndi nthenda ya chifuwa chachikulu (TB) m’dziko muno.

Wapampando wa komiti ya kunyumba ya malamulo yoona za umoyo, Dr Mathews Ngwale, ndi amene anayankhula izi munzinda wa Lilongwe pa mkumano omwe bungwe la Malawi Wellcome Liverpool Trust linakonza.

Bungweli limafuna kuuza aphunguwa mavuto omwe angabwerepo ngati ndalama zokwanira sizipezeka zolimbana ndi nthenda ya TB.

A Ngwale anati njira zina zopezera ndalama zopita ku umoyo ndi monga kumema kampani za insurance kuti zidzipereka ndalama zimene zimatolera napita nazo ku unduna wa zaumoyo.

Aphungu akuchita mkumano wawo

Iwo anati izi zili chomwechi kaamba kakuti anthu ambiri akachita ngozi amathamngira nawo m’zipatala zaboma pomwe kampanizi zimangoyika chidwi chake pokonza galimoto zoonongeka basi.

Sipikala wa nyumba ya malamulo, a Catherine Gotani Hara, anatsindika kuti iwo ngati aphungu akamema kofunikirako kuti ndalama zopita ku matendawa zichuluke.

Hara akuyankhula ndi olembankhani

Mkulu wa bungwe la Malawi Wellcome Liverpool Trust, Professor Henry Mwandumba, anati kafukufukuyi waululula kuti patha kukhala mavuto ambiri ngati ndalamazi sizingapezeke.

Ndalama zambiri zomwe zinkachoka ku boma la United States of America, zomwe pano zidasiya kubwera, zakhala zikuthandiza kwambiri kuti dziko lino lidzichita bwino polimbana ndi nthenda ya chifuwa chachikulu.

Olemba: Sam Phiri

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Kamtukule urges MSE to boost ownership shares awareness

Chisomo Break

RBM calls for Insurance Act review

MBC Online

Revamped railway hope for Lakeshore districts

Mayeso Chikhadzula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.