Mkulu wa apolisi m’chigawo cha kum’mwera mbali ya ku mvuma, a Noel Kayira, ati zigamulo zomwe mabwalo ena a milandu akupereka pa milandu yoononga chilengedwe zikukolezerabe m’chitidwe oyipawu chifukwa zikumakhala zofewa.
Izi zikudza pamene anthu amene akumawapeza olakwa monga omwe akusakaza chilengedwe m’phiri la Michiru m’boma la Blantyre akumalamulidwa kuti apereke chindapusa cha K20,000 yokha.
A Kayira amayankhula m’malo mwa mkulu wa apolisi m’dziko muno, a Merlyne Yolamu, pa mwambo okambirana za lamulo latsopano lomwe likupereka chigamulo chokhwima kwa anthu okuba zipangizo zamagetsi.
Iwo anapempha mabwalo a milandu kuti lamuloli aligwiritse bwino ntchito pomapereka zigamulo zokhwima kwa amene apezeka olakwa.
Olemba: Blessings Cheleuka