Akuluakulu a Religious Leaders Organisation apempha atsogoleri a mipingo m’dziko muno kuti achepetse kuyankhula kapena kuyika ndemanga pa nkhani zomwe zingayipitse mbiri komanso utsogoleri wadziko la Malawi.
Adindo a bungweli amayankhula izi mu nzinda wa Lilongwe pamwambo wa mapemphero omwe anachititsa popemphelera utsogoleri wa dziko lino komanso mavuto amene akuchitika monga imfa, ngozi zogwa mwadzidzidzi ndi kugwiritsa ntchito makina a internet molakwika.
A Muhammed Chindamba, amene ndi mkulu wa bungweli, apempha anthu ndi atsogoleri a mipingo kuti apewe kuyankhula ndi kufalitsa nkhani zopanda umboni.
Iwo anati kupanda kutero, zikhoza kusokoneza umodzi ndi mtendere wa dziko lino.
M’modzi mwa adindo a bungweli, m’busa Brian Nyirenda, anaonjezerapo kuti zimenezi zitha kubwezeretsa m’mbuyo ntchito za chitukuko m’dziko muno ndipo a Malawi akhale ogwirizana pofunira zabwino dziko lawo pamene likudutsa m’mikwingirima.