Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Amumanga pomuganizira kuti wapha mkazi wake chifukwa cha nsanje

Chataika Makawa wazaka 45 ali mchitokosi cha polisi ku Mangochi pomuganizira kuti wapha mkazi wake Esimy Daudi wazaka 42, amene amamukayikira kuti anali ndi chibwenzi.

Ofalitsankhani za polisi ya Mangochi, Amina Tepani Daudi, wati Makawa amumanga mmudzi mwa Kwitunji mdera la mfumu yaikulu Katuli dzulo pomuganizira kuti wapha mkazi wakeyo pomubaya ndi chikwanje kumsana.

Daudi wati mukafukufuku wawo, apolisi apeza kuti banjali linali lapendapenda chifukwa mamunayu amamulonda kwambiri mkaziyo pomuganizira kuti amayenda njila zamseli.

Makawa akaonekera ku khothi kukayankha mlandu wakupha.

 

Related posts

Apolisi agwira anthu awiri omwe akuwaganizira kuti amaba ku Area 25

Romeo Umali

STREET CARNIVAL FOR BREAST CANCER AWARENESS

MBC Online

MLW urges stronger public health and disaster preparedness to combat climate change impacts

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.