Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

‘Tisinthe kaganizidwe a Malawi’

M’busa Yassin Gama, yemwe amatumikira ku mpingo wa Mvama CCAP pansi pa Nkhoma Synod, wapempha aMalawi kuti akhale anthu olimbikira.

Pa ulaliki wawo ochoka m’buku la Yobu pa mapemphero wokumbukira kuti dziko la Malawi lakwanitsa zaka 60,  M’busa Gama anatsindika kuti ndikofunika a Malawi adzikhala ndi umunthu pomadzifunsa kuti Malawi wawo alibwanji.

“Yobu analibe chibwana ngakhale anadwala kwambiri, mabala thupi lonse koma adakanitsitsabe kutukwana Mulungu, zomwe mkazi wake anamuuza,” anatero Abusa Gama.

Pamenepa, iwo anachenjeza aMalawi kuti apewe kutembelera dziko lawo.

Mu uthenga wake, M’busa Esau Banda wa Pentecostal International Christian Centre analimbikitsa aMalawi kufunika kochilimika pokhala anthu a mtendere.

Mwambowu chaka chino ukuchitika ndi mutu woti ‘kuyendera limodzi mochilimika’.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Phungu ayendera zitukuko ku Chikwawa

MBC Online

Zomba communities awarded land certificates

Timothy Kateta

Salima Sugar ikupereka K500 million kwa osamuka m’minda yawo

Foster Maulidi
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.