Malawi Broadcasting Corporation
Crime Development Local Local News Nkhani

Nzika ziwiri zadziko la China azimanga zitakomola munthu

Apolisi ku Chikwawa amanga nzika ziwiri za dziko la China poziganizira kuti zamenya ndikukomola Silaj Maluwa wazaka 37 pomuganizira kuti anaba mafuta a galimoto.

Wachiwiri kwa ofalitsankhani zapolisi ku Chikwawa, Chancy Mfune, wati mzika za ku China-zo ndi Allen Cheng wazaka 37 ndi Peng Yongqia wazaka 35 omwe akugwira ntchito ku kampani ya zomangamanga yotchedwa Sinohydro, yomwe ikumanga malo a mthilira a Shire Valley Transformation.

Malinga ndi Mfune, ku kampaniyi kunasowa mafuta a galimoto ndipo anamuganizira Maluwa, yemwe amagwira ntchito yoyendetsa galimoto ku kampaniyi, kuti ndiye anaba mafutawo.

Anthu ena ogwira ntchito ku kampaniyi ndiwo anapeza Maluwa ali chikomokere ndipo anathamangira naye kuchipatala komwe akulandira thandizo la mankhwala.

#MBCDigital
#Manthu

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

VACANCY ANNOUNCEMENT

MBC Online

Mgwirizano wamphamvu pakati pa MACRA, ogwira nawo ntchito ndi ofunika — Kunkuyu

Simeon Boyce

Irrigation farming: A lifeline for needy students

McDonald Chiwayula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.