Apolisi kwa Makawa m’boma la Mangochi agwira Gladys Lingoni azaka 41 powaganizira kuti anatentha manja a mwana wawo wamwamuna wazaka zisanu ndi chimodzi chifukwa chokuti anadya ndiwo za soya.
Ofalitsa nkhani za Polisi ya Mangochi, a Amina Tepani Daudi ati mayiwa adathawa pa 1 mwezi omwe uno m’mudzi mwa Matuwi 2 kwa Mfumu yaikulu Mponda, komwe adasiya mwanayu ali mu ululu osasimbika.
“Mayiwa tikuwaganizira kuti anatentha mwana wawo manja onse awiri ndimajumbo chifukwa chakuti anadya ndiwo za soya zomwe anakonza kuti adyere nsima madzulo atsikulo,” anatero Daudi.
Mwanayo adalandira thandizo lamankhwala kuchipatala chaboma cha Mangochi koma anamutumiza kuchipatala cha Queen Elizabeth ku Blantyre kukalandira thandizo lapadera. Iwowa akayankha mulandu ofuna kuvulaza munthu.
Olemba Davie Umar