Achinyamata amene mmbuyomu amadalira kulandira mtukula pakhomo tsopano ndi odziyimira paokha chifukwa cha maphunziro a ntchito zamanja amene analandira kudzera ku bungwe la Comsip.
Goodson Zandana, amene adaphunzira ntchito ya utelala, komanso Saidi Carroti, amene adaphunzira ukalipentara ku dera la Benga 1 kwa mfumu yayikulu Mwadzama m’boma la Nkhotakota akuti m’makomo mwawo mavuto achepa.
Iwo anati izi zili chomwechi chifukwa akukwanitsa kupeza ndalama zimene akutha kugulira chakudya, zovala ndi zina zosowekera pakhomo.
Mkulu woona ntchito za Comsip m’boma la Nkhotakota, a Chimango Phiri, wati achinyamata 126 a m’bomalo aphunzira luso la ntchito zamanja zimenenso akuphunzitsa anzawo, kotero akuchepetsa vuto lakusowa kwa ntchito pakati pa achinyamata m’bomalo.
Mkulu oona zachitukuko ku khonsolo ya Nkhotakota, a Misheck Katudza, wati achinyamatawa akuphunziranso za ulimi wa makono kuphatikizapo kupanga manyowa a Mbeya kuti athane ndi vuto la njala m’makomo mwawo.
Olemba: Khadija Lapken