Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani

Aloza chala maboma akale posalabadira nsewu wa Karonga-Chiweta

Anthu ena adzudzula maboma a m’mbuyomu kaamba kosalabadira nsewu wa Karonga-Chiweta umene boma lapereka K5 billion ku kampani ya SOS Construction kuti awukonzenso.

Pothirapo ndemanga mu programme ya Nkhali pa MBC Radio 1, ena mwa anthuwo anati ndi zomvetsa chisoni kuti maboma apitawa sadaonetse chidwi chokonza komanso kusamalira nsewuwo, zimene anati zidapangitsa kuti ukhale ukuonongeka pakupita kwa nthawi.

A Maurice Msiska aku Chilumba m’boma la Karonga anayamikira President Dr Lazarus Chakwera pachitukukochi.

“Sitidaoneko utsogoleri omwe wachilimika kwambiri pa ntchito zachitukuko cha misewu kuphatikizapo kukonzanso nsewu wa Chiweta,” a Msiska anatero.

A Shadreck Mongola, amene amakhala kwa Nkhulambe m’boma la Phalombe, anati boma la President Dr Chakwera limaganizira zotukula dziko lino posaona nkhope.

“Ngakhale sindinadutseko nsewu umenewu, koma wakhala uli ofunikira kwambiri,”a Mongola adafotokoza motero.

Anthu ena mu programme yomweyi anati apitiriza kufotokoza kuti kukonzedwa kwa nsewu umenewu kudzathandizira kwambiri pa ntchito zachitukuko cha dziko lino kaamba kakuti katundu wambiri, kuphatikizirapo mafuta, adziyenda mofulumira kwambiri kuchokera m’dziko la Tanzania.

Mkulu wa bungwe la Road Transport Operators Association, a Bisani Banda, anati kukonzedwanso kwa nsewu umenewu kudzathana ndi vuto lakutchonatchona kwa galimoto zawo kaamba kakuonongeka kwa malo ambiri mu Chiweta.

A Banda anafotokozanso kuti izi zidzathandizira kuchepetsa ndalama zimene amagwiritsa ntchito pogulira zinthu monga mateyara ndi zipangizo zina za galimoto zimene zimawonongeka kaamba ka momwe nsewuwu wakhala uliri.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Gogo Chatinkha Maternity Ward wears a new face

MBC Online

RBM OPTIMISTIC OF CONTAINING INFLATION

Justin Mkweu

All set for Bridge Afric launch

Paul Mlowoka
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.