Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Alimi apeza misika ya ndalama zochuluka kuchiwonetsero chazaulimi

Bungwe la Malawi Confederation of Chambers of Commerce and Industry (MCCCI) lati alimi osiyana apeza misika ya ndalama zokwana K900 million pachiwonetsero cha zaulimi chomwe chatha kumapeto a sabata yapitayi.

Chiwonetserochi chinayamba pa 29 ndikutha pa 31 August ndipo chinatseguliridwa ndi mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera komanso mtsogoleri wa dziko la Mozambique Dr. Filipe Nyusi.

Mkulu owona za mamembala ku MCCCI, a Wezi Mungoni ati kupaturako kupeza misika alimiwa aphunzitsidwa zambiri ndi mabungwe monga Malawi Revenue Authority, Malawi Bureau of Standards, komanso Cannabis Regulatory Authority.

Alimiwa akuti apezanso mwayi odziwa zakapezedwe ka ndalama yochitira malonda komanso kapezedwe ka zipangizo zaulimi.

Chiwonetsero cha zaulimichi chimachitika chaka ndi chaka.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

YOUTHS PETITION PARLIAMENT ON ISRAEL LABOUR EXPORT INITIATIVE

Mayeso Chikhadzula

Onani to contest for MCP Director of Youth

Sothini Ndazi

Chilima leaves for Tanzania

Beatrice Mwape
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.