Malawi Broadcasting Corporation
News Nkhani

Bushiri wagawa chimanga kwa anthu oposa 18,000

Anthu oposa 18,000 okhala mumzinda wa Lilongwe alandira chimanga chaulere lamulungu kuchokera kwa mtsogoleri wa mpingo wa Enlightened Christian Gathering the Jesus Nation,  Prophet Shepherd Bushiri.

Bushiri wagawa chimangachi kulikulu la office yampingowu ku Golden Peacock komwe kunafika anthu ochokera mmadera monga Kauma, Chilinde, Kawale, Senti, Chimoka, Mtandire ndi ena ambiri.

Mmawu ake, Bushiri wati ndi okondwa kuti ntchito yogawa chimangachi ikuyenda bwino.

“Ndine osangalala kuti anthu ambiri omwe akusowa chakudya m’madera ozungulira tawuni ya Lilongwe alandira nawo thandizoli ndipo ndikulimbitsa onse akufuna kwabwino kuti tigwirane manja populumutsa miyoyo ya a Malawi anzathu omwe akuvutika ndi njala,” watero Bushiri.

Pakadali pano, anthu am’maboma a Mzimba, Karonga, Nkhotakota, Ntcheu, Lilongwe, Rumphi, Mulanje, Thyolo, Zomba, Nsanje ndi Nkhatabay ndi omwe alandira thandizoli.

Ntchitoyi ipitilirabe mmaboma ena komwe njala yafika povuta kwambiri.

Related posts

Malawi geared to fight HIV drug resistance

Romeo Umali

Govt committed to transforming Malawi – Chimwendo Banda

Rabson Kondowe

EX-SULOM BOSS IN NOMADS CAMP  

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.