Apolisi ku Chiradzulu akufunafuna Steven Museu pomuganizira kuti wapha bwenzi lake lazaka 40, Bertha Nkolimbo.
Izi zachitika mmudzi wa Liphuthu, mfumu yaikulu Nkalo m’boma lomwelo la Chiradzulu. Ofalitsankhani wapolisi ku Chiradzulu, Cosmas Kagulo, wati malemuwo anachoka pa 17 June kupita kokamwa mowa koma sanabwelerenso.
Asanasowe, anthu ena anati anamuona Bertha ali kunyumba kwa Museu. Ndipo tsiku lotsatira, woganiziridwayo anatenga nsapato za malemuyo kukasiya ku malo omwera mowa ndikuuza mwini malowo kuti adzamupatsire nsapatozo Bertha kenako Museu sanaonekenso mmudzimo mpaka pano.
Anthu omwe anapita kukakumba manda mmudzimo ndiwo apeza thupi la malemuwo koma litawonongeka. Ndipo zotsatira za chipatala zawonetsa kuti malemu Bertha wafa atavulala mmutu.