M’busa Clifford Kawinga, amene ndi mtsogoleri wa mpingo wa Salvation for All Ministries, walimbikitsa mafumu m’boma la Mchinji kuti adzikhulupilira komanso kupempha nzeru kwa Mulungu, mmalo modalira zikhulupiliro zamakolo ndi zitsamba.
A Kawinga ayankhula izi pa sukulu ya pulaimale ya Zulu, mdera la Mfumu yaikulu Zulu, komwe agawa mawu a Mulungu komanso matumba a chimanga oposera 4,000 kwa anthu ochekera mdera la Mfumu yaikulu Zulu, m’bomali.
Iwo aperekanso ma baibulo kwa mafumu mderali chifukwa anati anthu akuyenera kukhala m’moyo wa pemphero komanso kuthandizana, maka mu nyengo imene akuti anthu ena akusowa chakudya kaamba ka ng’amba imene inakhudza dziko lino.
“Kuthandiza amene alibe sizitengera kuti uli ndi chuma kapena zinthu zochuluka. Tisadikire munthu wochekera kunja kudzathandiza ife kuno,” iwo anatero.
Mfumu yaikulu, Zulu inathokoza Apostle Kawinga kaamba thandizolo.
Mfumuyi inachenjeza kuti athana ndi mafumu amene apezeke akuchita chinyengo kapena kulanda chakudya chimene anthu alandira kuchokera kwa a Kawinga.