Kampani ya Airtel Malawi siyinapange phindu lililonse chaka chatha ndipo m’malo mwake, yataya ndalama (loss) za pakati pa K15.1 billion mpaka K15.7 billion.
Izi ndimalinga ndi kalata yochokera ku Airtel yonena m’mene akuwonera kuti chuma cha kampaniyi chayenda bwanji chaka chatha.
Kalatayi ikudza Airtel Malawi itawerengeranso za chuma chake cha chaka chatha.
Kalata yoyamba inaawonetsa kuti kusapanga phinduku kunali pa K2 billion koma kalata yatsopanoyi ikuti kwakwera atawonkhotsera ndalama zina zama dollar zokhudzana ndikubwereka zipangizo zothandizira ntchito yawo.
Airtel Malawi ndi imodzi mwa kampani za lamya m’dziko muno zomwe ziri pa msika wamasheya wa Malawi Stock Exchange.