Malawi Broadcasting Corporation
Business Development Local Local News

A Malawi First sachitanso zionetsero zotsutsana ndi chizindikiro cha tax stamp

Gulu la Malawi First molumikizana ndi bungwe la Malawi Revenue Authority ati zionetsero zomwe anakonza a Malawi First zokhudza msonkho wa tax stamp sizichitika.

Izi zikutsatira zokambirana zomwe anali nazo kummawaku pakati pa bungwe la MRA, Malawi First ndi oyimira mabizinesi ang’onoang’ono.

Gulu la Malawi First linakonza zionetsero mwazina zosagwirizana ndi mnsonkhowu ati kaamba koti mnsonkhowu upsinja mabizinesi ang’onoang’ono.

Pa zokambilanazi a Malawi First agwirizana ndi mfundo za MRA kuti tax stamp ithandizira kuthetsa mchitidwe olowetsa katundu mozembetsa, wina owopsya ku miyoyo ya anthu uthe. Iwo ati pakhala zokambilana zina mtsogolomu ndi unduna wa zachuma komanso wa malonda za mnsonkhowu koma pakali pano mnsonkhowu wayamba waimitsidwa kaye.

A Bon Kalindo mtsogoleri wa Malawi First, a Owen Belo oyimira mabizinesi ang’onoang’ono komanso a Steven Kapoloma oimira Bungwe la MRA ndi amene asayanira mgwirizanowu kuti asachite zionetsero zotsutsana ndi mnsonkhowu.

Ochita mabizinesi ang’onoang’ono akhala akudandaula kuti katundu yemwe amalowa mdziko muno mozembetsa akusokoneza bizinesi zawo.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

PAC urges unity in fight against smuggling

McDonald Chiwayula

TNM strengthens internet connectivity

Stephen Dakalira

Ntchito yofufuza ndege m’dziko la Russia yayamba

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.