Apolisi ku Lilongwe agwira a Rodney Kandulu a zaka 25 zakubadwa powaganizira kuti anawononga ndalama zokwana K18 million za kampani ya Premier Bet, komwe amagwira ntchito, poyichitila juga pa masewero otchedwa ‘Navigator’ mu ofesi mwawo.
Ofalitsa nkhani ku Polisi ya Lilongwe, a Hastings Chigalu, ati a Kandulu, omwe amagwira ntchito ngati otolera ndalama ku ofesi ya Premier Bet ya ku Area 3, anapalamula mlanduwu pa 4 August 2024, lomwe linali tsiku Lamulungu.
Atatolera ndalama zomwe ofesi yawo inapanga patsikuli, iwo anayamba kuzitchovera juga n’cholinga chofuna kupeza phindu.
Koma itakwana 12 koloko masana, mabwana awo anapeza kuti ndalama ina ikusowa ndipo bambowa anawapeza kuti amachita zinthuzi pa foni yawo ndipo apolisi anathamangira kumaofesiko kudzawanjata.
Poyankha mafunso kwa apolisi, a Kandulu anavomereza kulakwa kwawo ndipo anati ndi achisoni chifukwa sangakwanitse kubweza ndalama zonsezo.
Iwo akawonekera ku bwalo la milandu posachedwapa kuti akayankhe mlandu okuba pa ntchito.
A Kandulu ndi ochokera m’mudzi mwa Bismark m’dera la mfumu Kapeni m’boma la Blantyre.