Ochita malonda a zovala zakaunjika mu mnzinda wa Lilongwe akuchita zionetsero kamba kakukwera kwa misonkho pa mabelo a zovalazi.
Pakali pano, ochita malondawa afika pa ofesi ya bungwe lotolera misonkho ya Malawi Revenue Authority (MRA) komwe akudzatula zikalata zawo zamadandaulo.