Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

‘Ndondomeko ya NEEF isintha miyoyo ya ambiri’ — Chakwera

Mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, wati awonetsetsa kuti anthu amene akuchita malonda m’misika ya mdziko lino akupindula kudzera mu ndondomeko yobweleketsa ndalama ya NEEF.

A Chakwera anena izi loweruka ku Mzuzu pamene amayendera ochita malonda pa msika wa Mzuzu komanso Zigwagwa.

Mtsogoleri wa dziko linoyu anati pakali pano, boma laika ndalama zoposa K80 billion zoti zithandizire anyamata komanso amayi omwe akuchita malonda ngati mbali imodzi yoonetsetsa kuti akhale odzidalira pa chuma.

A Chakwera kugula ena mwa malonda pa msika wa Mzuzu

Pa nkhani ya ndalama za ngongole ya NEEF, zomwe ena anakanika kubweza, A Chakwera anati akuzindikira bwino lomwe za mavuto omwe anthuwa anakumana nawo kaamba ka matenda a Covid-19.

Iye anati ngakhale izi zili chomwechi koma boma lake lipitiriza kutukula miyoyo ya anthu ambiri m’dziko muno kudzera mundondomekoyi.

Phungu wamzinda wa Mzuzu, a Bennex Mwamulima, anayamikira zomwe boma likuchita ku Mzuzu motsogozedwa ndi Dr Chakwera.

Wapampando wa mavenda ku msika wa Mzuzu, a Alexander Sikwese, anati anthu ochita malonda akachita bwino dzikonso limachita bwino.

“Bwana ndithokoze poti mwakhala Mtsogoleri woyamba kutiyendera mavenda kuno ku Mzuzu mu mbiri ya dziko lino, ndikukhulupilira kudzera mu ndondomeko ya NEEF zinthu zambiri zisintha,” Anatero a Sikwese.

Wolemba: Jackson Sichali

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

‘Musalole andale kukutumani kuti muchite ziwawa’

MBC Online

Masewero a Darts m’chigawo chapakati apeza thandizo

Foster Maulidi

A Sendeza alimbikitsa chilungamo pa ndondomeko ya Mtukula Pakhomo

Lonjezo Msodoka
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.