Bungwe la asilamu la Muslim Association of Malawi (MAM) lati mwezi otsiriza kusala kudya wa Ramadan sunaoneke, choncho iwo ati Eid idzakhalapo lachinayi.
Mneneri wa bungweli, Sheikh Dinala Chabulika, auza MBC kuti zateremu ndiye kuti asilamu atsiriza kusala kudya mawa lachitatu ndipo tchuthi cha Eid chidzachitika lachinayi likudzali.