Akuluakulu a mpingo wa CCAP mu synod ya Livingstonia akukumana ku Embangweni ku tchalichi cha Laudon m’boma la Mzimba.
Moderator wa Mpingowu M’busa Rueben Msowoya akuyembekezeka kutula pansi udindowu ndipo mmalo mwake M’busa Jairos Kamisa ndi amene atenge udindo wa Moderator watsopano.
Nthumwi zikuyenera kuchita chisankho chosankha moderator amene adzatenge udindowo mchaka cha 2026.
Pamapeto pa mkumanowu moderator mogwirizana ndi komiti yayikulu akuyembekezeka lkusankha adindo atsopano amene agwire ntchito m’mipingo, nthambi ndi mabungwe onse a synodiyi kwa zaka ziwiri zikubwerazi.
Pamwambowu pafika akukuakulu a boma kuphatikizapo Sipikala wanyumba yamalamuro a Catherine Gotani Hara, nduna yaza ulimi a Sam Kawalex ndi alendo ena osiyanasiyana.
Olemba Hassan Phiri