Apolisi ku Mangochi amanga Dalitso Nkutu, 19, pomuganizira kuti wabaya ndi mpeni bwenzi lake amene amamuganizira kuti akuzemberana ndi amuna ena.
Mneneri wa polisi ku Mangochi, a Amina Tepani Daudi, ati izi zachitika m’mudzi wa Chindamba kwa mfumu yaikulu Chowe m’bomali.
A Daudi ati awiriwa ali pa chibwenzi chodziwika ku makolo ndipo anagwirizana zozakwatirana mtsogolo koma mnyamatayu wakhala akumva mphekesera kuti bwenzi lakelo limakumananso ndi amuna ena.
Iwo ati Lachitatu, mnyamatayu anauzidwa kuti bwenzi lake lagona kwa mamuna wina ndipo atamutsatira ndi kukamutengera ku nyumba kwake, mkangano unabuka mpakana anamubaya mtsikanayo m’mutu ndi pamwendo.
Zitatha izi, Nkutu anakadzipereka yekha ku polisi ya Malaya pozindikira kuti analakwitsa, ndipo apolisiwo anamutumiza ku polisi ya Mangochi.
Iyeyu akaonekera ku bwalo lamilandu kukayankha mulandu ofuna kuvulaza munthu.