Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Kugulitsa kapena kupanga katundu osayezedwa ndi mulandu – MBS

Ngati njira imodzi yofuna kupititsa patsogolo ntchito za milingo mdziko muno, bungwe loona za milingo la Malawi Bureau of Standards lati linakhazikitsa ndondomeko yopereka mphatso ya ndalama zokwana K50,000 kwa yemwe angawatsine khutu zamchitidwe ogulitsa kapena kupanga katundu mosatsatira malamulo a bungweli.

Izi zadziwika pomwe  bungweli linachititsa maphunziro osula atolankhani za kalembedwe kankhani zokhudza milingo ku Salima.

Mkulu wa Bungweli, a Benson Thole,  ati zina mwanjira zomwe anthu angatsate ndi monga kulemba kalata kwa mkulu wa bungweli kapena kuimba foni pa 462 kapena 842.

A Thole anati kugulitsa kapena kupanga katundu osayezedwa mlingo ndi mlandu waukulu kaamba koti khalidwe lotere limapereka chiopsezo kumiyoyo yawanthu

 

Olemba:  Mphatso Tebulo

Related posts

GOVERNMENT SECURES $350 MILLION FROM MCC

MBC Online

MBC SIGNS PACT ON AIRING EXCLUSIVE SIGN LANGUAGE PROGRAMMES

MBC Online

We do not want to lose points — Msukwa

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.