Lameck Gamphani ndi Wongani Lungu awasiya pa m’ndandanda wa osewera a FCB Nyasa Big Bullets pamene akuyembekezera kuti akathambitsane ndi timu ya m’dziko la Zambia ya Red Arrows mu mpikisano wa CAF Champions League Lamulungu likubwerali.
Masewerowa adzachitikira pa bwalo la masewero la Bingu mu mzinda wa Lilongwe ndipo achibwereza adzakhalapo sabata ikubwerayo mu mzinda wa Lusaka m’dziko la Zambia.
Osewera awiriwa angofika kumene ku timu ya Bullets kuchokera ku matimu a Premier Bet Dedza Dynamos ndi Mzuzu City Hammers.
Mkulu wa timu ya Bullets, a Albert Chigoga, ati osewerawa akanika kukhala nawo pa m’ndandandawu kaamba ka kuti anabwera kalembera wa osewera mu mpikisanowu atatha kale.
Komabe, a Chigoga ati osewerawa awalembetsa mu gawo lachiwiri la mpikisanowu ngati timu yawo ingagonjetse Red Arrows ndi kupita mu ndime ina.
Opambana masewerowa, adzakumana ndi timu ya TP Mazembe ya m’dziko la Democratic Republic of Congo.
Olemba: Praise Majawa