Mkulu watsopano wa Polisi ya Limbe, a Edwin Mkhambo, watsimikizira anthu ochita malonda mderali komanso madera ozungulira kuti aonetsetsa kuti kuli chitetezo chokwanira.
A Mkhambo anena izi pa msonkhano wa atolankhani komwe anatsindika kuti ntchito yoika ma camera othandizira kukhwimitsa chitetezo (CCTV camera pachingerezi), ikuthandiza kwambiri.
A Mkhambo alowa mmalo mwa a Gladwell Chipumphula, amene pano ndi wachiwiri kwa komishanala wa apolisi kuchigawo cha kummawa.
WOLEMBA: GHWABUPI ANGELA MWABUNGULU


