Atsikana komanso amayi achichepere ambiri mdera la T/A Chiwalo m’boma la Phalombe akuti tsopano akutha kupeza thandizo la kulela komanso uchembere wabwino mosavuta.
Izi zikutsatira ntchito ya Her Voice Fund imene bungwe la Coalition of Women Living with HIV/AIDS (COWLHA) ikugwila yolimbikitsa achinyamata kuti adzitha kulela komanso kuchita uchembere wabwino.
Oyendetsa ntchitoyi, a Edwin Nyoka, ati akwanitsa kusintha machitidwe achipatala kwa achinyamatawa akafuna thandizo la kulera m’zipatala zimene ati zimabwenzeretsaa m’buyo ntchito za kulera pakati pa achinyamata.
A Nyoka ati, pakadalipano, mafumu m’derali atenga udindo ofalitsa uthenga wa kufunika koti achinyamatawa adzilera komanso kupeza thandizo la uchembere wabwino mosavuta m’zipatala.
Kupatula izi, bungweli likulimbikitsanso ntchito yoyezetsa khomo la chibelekero pakati pa atsikana ndi amayi achichepere, chifukwa chachikulu cha TB komanso kachilombo Ka HIV.
Bungweli lati likuphunzitsanso achinyamatawa kuti afikire anzawo ndi uthengawu poonjezera pa ntchito yowalimbikitsa kuti adzitha kudziyankhulira m’magawo omwe sakuyenda bwino.
Ntchito ya Her Voice Fund inayamba m’chaka cha 2024 ndipo itha chaka cha mawa.

