Malawi Broadcasting Corporation
Local News Nkhani

Munthu mmodzi wavulala modetsa nkhawa pa ngozi ya sitima

Munthu mmodzi wavulala modetsa nkhawa pa ngozi ya sitima ku Blantyre mu njanji ya Magalasi – Nyambadwe – kudutsa ku Chapima.

Ofalitsankhani za polisi ya Ndirande, a Maxwell Jailosi, ati adakafufuzabe za nkhaniyi ndipo a kampani ya CEAR, omwe ndi eni sitimayi, sanapezeke kuti ayankhulepo pa nkhaniyi.

Koma malinga ndi anthu amene akuti anawona ngoziyi ikuchitika, munthuyu anadumpha mu sitimayi, yomwe inali ikuyenda, pamene ena akuti amayesera kukwera sitimayi ikuyenda.

Munthuyu akulandira thandizo la mankhwala pa chipatala cha QECH.

Olemba: Blessings Cheleuka

Related posts

President Chakwera awonekera m’nyumba ya malamulo

Romeo Umali

S.I.N.A drops debut single

Romeo Umali

Burning Spear jets in Malawi

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.