Bungwe la Surveyors Institute of Malawi lati chilichonse chili mchimake pa zokonzekera za msonkhano wawo waukulu wapachaka umene uyambe pa 26 mpakana pa 27 mwezi uno.
Mlembi wamkulu wa bungweli, a Bernard Mleta, ndi amene amayankhula izi Lachiwiri masana atalandira thandizo la ndalama zokwana K3 million kuchokera ku kampani ya Property Solutions Limited.
A Mleta anayamikira kampaniyi kaamba ka thandizoli chifukwa laonetsa poyera kuti ali ndi chidwi chokweza ntchito zabungweli.
Mkulu wa Property Solutions, a Willy Mwawa, anati athandiza chifukwa akudziwa zakufunika kwa mwambowu komanso ngati membala wa bungweli, ndi udindo wawo kutero.
Kampaniyi imagwira ntchito younika kuchuluka ndi mlingo wa zinthu kapena malo m’dziko muno.