Olimbikitsa ufulu wanyama m’dziko muno, a Dominic Nyasulu, ati ziweto zambiri anthu akuzichitira nkhanza kaamba kakuti ambiri samadziwa kuti ziweto nazo zili ndi ufulu ndipo zimayenera kutetezedwa ku nkhanza.
A Nyasulu amayankhula izi mu mzinda wa Lilongwe pamene amawunikira olemba nkhani kuti adziwitse anthu zakuyipa kochitira nkhanza ziweto.
Iwo anati kusunga ziweto malo amodzimodzi, kuzimanga pa chingwe, kumenya ndi kuzipatsa madzi akuda ndi nkhanza ndipo anawonjezeranso kuti pakadali pano akudikira boma limalizitse kuwunikira lamulo loteteza ziweto ku nkhanza zoterezi.
Katswiri pa maphunziro a moyo wa nyama ku sukulu ya LUANAR, a Jonathan Tanganyika, anati ndiwo ya nyama yambiri siyikoma chifukwa imakhala kuti yakumana ndi nkhanza zambiri.
A Tanganyika anati kupha chiweto pomwe zina zikuonelera ndi nkhanzanso chifukwa zimasokoneza ubongo wa nyama yoona zoterozo.