A Saudi Fund for Development ati afulumizitsa ntchito yojambula msewu wa Makanjira ku Mangochi kuti ntchito yomanga msewuwu iyambe mwachangu.
Izi akuti zikutengera chidwi chomwe boma la Malawi likuonetsa pofuna kuthandiza mayendedwe a anthu aku Makanjira.
Wachiwiri kwa mkulu wa Saudi Fund for Development, a Faisal Al-Kahtani, amalankhula ii mu mzinda wa Washington DC pamene anakumana ndi nduna ya zachuma, a Simplex Chithyola Banda, amene akuchita nawo msonkhano waukulu wa zachuma padziko lonse.
A Chithyola Banda akuti boma laika chidwi chonse kuti nsewu umenewu ukonzedwe poti kwa nthawi yaitali anthu akhala akudikira za nseu umenewu kuti ukhale waphula.