Khothi la Magistrate mu mzinda wa Blantyre la lamula kuti abambo atatu akagwire ukayidi kwa zaka ziwiri komanso chaka ndi theka kaamba kopezeka olakwa pochita malonda ogulitsa makala opanda chiphaso komanso kuzembetsa zinthu za munkhalango.
Popereka chigamulo, Magistrate Godfrey Balaka anati zilango zonsezi ziyendera limodzi pofuna kuti anthu ena atengerepo phunziro ndipo mlanduwu adapalamula pa 17 April, 2024.
Nthambi za boma monga Police, ACB ndi nthambi ya zankhalango padakali pano zikugwira limodzi ntchito yothandiza kuteteza zachilengedwe.
#MBCDigital
#Manthu