Boma likukhazikitsa mtukula pakhomo wammizinda lero.
Ntchito yokhazikitsa ntchito ya mtukula pakhomo wa mmizinda,imene ndiya ndalama zokwana K15.7 billion, ili mkati mu mzinda wa Zomba.
Kudzera mu ndondomekoyi, mabanja okwana 105,000 alandira ndalama zokwana K150,000 pakamodzi kuti alimbane ndi umphawi.
Nduna ya zachuma, a Simplex Chithyola Banda, nduna yoona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo, a Jean Sendeza, komanso mlembi wa zachuma Professor Betchani Tchereni, ali nawo pa mwambowu.