Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

‘Yambani ma bizinesi ang’ono ndi mtukula pakhomo’

Ena mwa anthu omwe akupindula ndi ndondomeko ya Mtukula Pakhomo m’boma la Salima ayamika boma kaamba ka ndondomekoyi, yomwe akuti ikuwathandiza kusamalira makomo awo makamakanso ana a sukulu.

Iwo ayankhula izi nduna ya za chisamaliro cha anthu, a Jean Sendeza, amayendera ena mwa mabanja omwe ali mu ndondomeko ya mtukula pakhomo m’mudzi wa Chingongo, mdera la mfumu yaikulu Salima.

Mayi Patuma Jailosi, omwe ali ndi ana anayi, analandira K101,200 zomwe akuti pambali pogulira zofunikira za ana kusukulu, analowa mugulu lina la banki nkhonde, yomwe imapereka mwayi kwa amayi osungitsa komanso kuchulukitsa ndalama zawo.

Nawo Gogo Chipazala akuti akwanitsa kugula unifomu, nsapato komanso makope ana atatu omwe akusunga, atalandira K80,000.

Padakali pano, chiwerengero cha anthu omwe akupindula ndi ndondomekoyi m’boma la Salima chikuposera 12,000, kukwera kuchoka pa 8,000.

M’boma la Salima, Mtukula Pakhomo inayamba m’chaka cha 2008.

A Sendeza alimbikitsa anthuwa kuti adzichita mabizinesi ang’ono komanso alowe mmagulu a banki nkhonde kuti miyoyo yawo itukuke ndikuti adzitha kugula zofunika za ana a sukulu.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

TNM Super League mid-season Analysis

Romeo Umali

Man arrested in Neno for possession of coffins

MBC Online

Chithyola Banda, Tchereni litmus test

Justin Mkweu
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.