Unduna wa zantchito, watseka mbali ina ya Makandi Tea Estate imene ili m’boma la Thyolo chifukwa chophwanya ena mwa malamulo antchito.
Mbaliyi ndi kumene kuli minda ya tiyi ndipo kumadziwika kuti ku 17 A.
Mwazina, a Mumba apeza kuti pamalopa, palibe madzi aukhondo, zimbudzi komanso ogwira ntchito ake alibe zipangizo zowatetezera pamene akugwira ntchito yawo.
Pakadali pano, ndunayi yapereka masiku asanu ndi awiri kuti kampaniyo ikhale itakonza zolakwikazo komanso alamula eni kampaniyo kuti apereke malipiro onse a ogwira ntchito kumbali yomwe ayitsekayi ngakhale kuti sakugwira ntchito.
Mmodzi mwa akuluakulu a kampaniyo, a Joe Palani, ati ayetsetsa kukonza zonse zolakwika mmasikuwo.
A Mumba akuyendera kampani za m’chigawo cha ku m’mwera potsatira madandaulo amene anthu ochuluka kuphatikizapo ogwira ntchito m’malowa akhala akupereka.