Unduna waza umoyo wati walandira katemera wa matenda a cholera 720,185 wa mkamwa kuchokera ku bungwe laza umoyo pa dziko la World Health Organization (WHO).
Mneneri ku unduna waza umoyo, a Adrian Chikumbe, anena zimenezi pomwe zadziwika kuti anthu ena m’maboma a Chitipa, Karonga, Balaka komanso Machinga apezeka ndi matenda wotsekula m’mimba a kolera.
A Chikumbe ati akugwira limodzi ntchito ndi ma unduna osiyanasiyana ndi mabubgwe okhudzidwa pofuna kudziwitsa anthu momwe angalimbanilane ndi matendawa.
Malinga ndi a Chikumbe, katemera amene alandira amupereka m’maboma onse omwe mwabuka matenda a kolera.