Bungwe la Malawi Red Cross Society (MRCS) lati lipitiriza ntchito yake yolumikizitsa nzika zomwe zinathawa kwawo zomwe zikukhala pa msasa wa Dzaleka kuti zidzilumikizana komanso kukumana ndi abale awo.
Mlembi wamkulu ku bungweli a Chifundo Kalulu ayakhula izi pa msasa wa Dzaleka pomwe bungweli limaunikila nzika zomwe zinathawa kwawozi momwe zingatsatire ndondomeko zothandizira kulumikizana ndi abale awo mwaulere.
Iwo ati kuchokera pomwe bungweli linakhazikitsa ndondomekoyi mchaka cha 2012, bungwe la Malawi Red Cross lakwanitsa kulumikizitsa anthu ambiri ndi abale awo.
M’modzi mwa akuluakulu ku nthambi ya boma yoona za anthu omwe anathawa kwawo a Amos Mkandawire ayamikira bungwe la Malawi Red Cross pokhazikitsa ndondomekoyi ponena kuti ithandizira ana amasiye omwe ali pa msasawu kuti athe kulumikizana ndi abale awo ku maiko a kwawo.
Olemba: Madalitso Mhango