Malawi Broadcasting Corporation
Crime News Nkhani

TIMASOWEKERA ZIPANGIZO ZOJAMBULIRA KANEMA

Akatswiri ochita zisudzo omwe ali mukanena wotchedwa “School Days” apempha anthu kuti aziwathandidza ojambula makanemawa maka panthawi yomwe akujambula komanso akutulutsa kanema watsopano.

Tumpe Mtaya yemwe watchuka ndi dzina loti Phwedo wati amavutika kupeza zipangizo zojambulira, ndalama komanso malo okuti ajambulire kanemayo popeza anthu ena amakaniza malo awo.

Tupe Mtaya (Phwedo)

Amos Filisa yemwenso anali mukanemayu ndi dzina loti Mphatso wapempha anthu kuti azimuona nthawi zonse ngati iyeyo popeza sanasinthe ndipo asamadabwe naye akamapanga zinthu zina.

Mwa akatswiri ena omwe anachita nawo kanemayu ndipo anayankhula ndi mkozi wa mapologalamu a MBC 2onthego anali, Yvonne Jane Chanache (Leticia), Amosi Filisa (Mphatso), Tumpe Mtaya (Phwedo) ndi Ruben Matiki ( Wachigalimoto).

Akatswiri amukanema wa School Days akhala ali mumzinda wa Blantyre ku hotela ya Amaryllis kukumana ndi anthu komanso kuwonetsa kanemayu. Padakali pano, anthu oposa 1 miliyoni amuwonera kale kanemayu pamakina a intaneti (YouTube) chimuyikireni masabata atatu apitawo.

Wolemba: Emmanuel Chikonso

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

“Ntchito zomangamanga zidzikhala zapamwamba”

Mayeso Chikhadzula

MBC holds corruption and fraud awareness for staff

MBC Online

Financially help people with dwarfism, analyst plead

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.