Bungwe la Technical Entrepreneurial Vocational and Education Training Authority (TEVETA) likulingalira zolimbikitsa ndondomeko yofuna kuti maphunziro a ntchito za manja afikire anthu onse.
Wapampando wa bungweli, a Pyoka Tembo, amayankhula izi m’boma la Mulanje pamene amapereka malo ophunzirapo ntchitoyi otchedwa Ndanga, amene anawakonzanso atawonongeka ndi namondwe wa Anna ndi Gombe.
A Tembo anati achinyamata okhawo a luso ndi omwe angakwanitse kuthandidzira pa chitukuko chadziko lino.
M’modzi mwa amene watsiliza maphunziro a ulimi wa nkhumba, a Mary Maseko, anati maphunziro awo awapatsa kuthekera koti apeze phindu loyenelera mu ulimi wawo.
Pa mwambowu, TEVETA inaperekanso masitifiketi kwa anthu 125 omwe atsiriza maphunziro a ntchito zamanja monga zomangamanga, zaulimi wa nkhumba ndi luso losoka zovala.